Isaiah 17

Uthenga Wotsutsa Damasiko

1Uthenga wonena za Damasiko:

“Taonani, mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda,
koma udzasanduka bwinja.
2Mizinda ya Aroeri idzakhala yopanda anthu
ndipo idzakhala ya ziweto, zimene zidzagona pansi
popanda wina woziopseza.
3Ku Efereimu sikudzakhalanso linga,
ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu;
Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu
monga anthu a ku Israeli,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.

4“Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobo udzazimirira;
ndipo chuma chake chidzasanduka umphawi.
5Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu
umene anatsiriza kukolola.
Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu
anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
6Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale
monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni
kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi
mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,”
akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.

7Tsiku limenelo anthu adzayangʼana Mlengi wawo
ndipo adzatembenukira kwa Woyerayo wa Israeli.
8Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe,
ntchito ya manja awo,
ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera,
ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga.
9Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja.

10Inu mwayiwalatu Mulungu Mpulumutsi wanu;
simunakumbukire Thanthwe, linga lanu.
Choncho, ngakhale munadzala mbewu zabwino,
ndi kuyitanitsa kunja mitengo ya mpesa,
11nimuyembekeza kuti zikule tsiku lomwelo
ndi kuphukira maluwa mmawa mwake,
komabe zimenezi sizidzakupindulirani
pa tsiku la mavuto.

12Aa, mkokomo wa anthu a mitundu yambiri,
akusokosa ngati kukokoma kwa nyanja!
Aa, phokoso la anthu a mitundu ina,
akusokosa ngati mkokomo wa madzi amphamvu!
13Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri,
koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula.
Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri,
ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe.
14Pofika nthawi yamadzulo zoopsa zidzayamba kuchitika,
ndipo zidzakhala zitatha pofika mmawa.
Izi ndizo zidzachitikire anthu otilanda zinthu,
gawo la amene amatibera zinthu zathu.
Copyright information for NyaCCL